Siwe Wekha

Siwe Wekha

Taimon Tipa

Taimon

Ooh oooh ooh ooh!

Ukamalimbikira Ulendo

Sungathere panjira

Ukudutsa muzopinga

Tsiku lina utulukira

Munthu ukamafika poiphula

Umakhala wakhaula

Achuluka okudelera

Ena okukhomelera

Mtima wako watopa

Thupi lako lafooka

Pena ngati ungozisiya

Koma tiye

Ndi ambiri okudalila

Ndipo akuchulukira

Ukazisiya adandaula iwe tiye

Inde zambiri zakanika

Aaah eeh siwe wekha

Ifeso takanika aaah

Eeh siwe wekha koma

Ndife akulu akulu

Zosatheka kumangolira

Koma nafe tikudutsa

Momwemo aah eeh siwe wekha

Timadziwa mwanawe ndiwe

Olimbikira koma tilibe

Nthawi yokuombera m'manja

Ena sakondwera kukuona

Ukupita amatchinga njira

Kuti usapeze podutsa eeeh

Amangokhumba atakhala

Yaweh ayimitse zako

Zisayende dziko lonseli

Adzisangalala okha

Koma osamadzilembera

Malile moyo uno ndi

Vala zilimbe okhulupilira

Tonse tidzidikira

Mtima wako watopa

Thupi lako lafooka

Pena ngati ungozisiya

Koma tiye ndi ambiri

Okudalira ndipo akuchulukira

Ukazisiya adandaula iwe tiye

Inde zambiri zakanika

Aaah eeh siwe wekha ifeso

Takanika aah eeh siwe

Wekha koma ndife akulu

Akulu zosatheka kumangolila

Koma nafe tikudutsa

Momwemo aaah eeh siwe wekha

Inde zambiri Zakanika

Aah eeeh siwe wekha ifeso

Takanika aah eeh siwe

Wekha koma ndife akuluakulu

Zosatheka kumangolira koma

Name tudutsa momwemo

Aah eeh siwe wekha

Siwe Wekha

Siwe Wekha

Taimon Tipa

00:00 / 00:00